1. Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ace,
2. Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paskha ufika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kupacikidwa pamtanda.
3. Pomwepo anasonkhana ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ku bwalo la mkuru wa ansembe, dzina lace Kayafa;
4. nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi cinyengo, namuphe.
5. Koma ananena iwo, Pa dzuwa la cakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.
6. Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,
7. anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa yaalabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatari, nawatsanulira pamutu pace, m'mene Iye analikukhala pacakudya.
8. Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?