Mateyu 25:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma pakati pa usiku panali kupfuula, Onani, mkwati! turukani kukakomana naye.

7. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao.

8. Ndipo opusa anati kwa ocenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; cifukwa nyali zathu zirikuzima.

9. Koma ocenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.

10. Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo, analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.

Mateyu 25