Mateyu 22:34-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.

35. Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,

36. Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?

37. Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

38. Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba.

Mateyu 22