Mateyu 22:33-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi ciphunzitso cace.

34. Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.

35. Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,

36. Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?

37. Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

38. Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba.

39. Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

40. Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.

41. Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,

42. nati, Muganiza bwanji za Kristu? ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.

Mateyu 22