Mateyu 22:25-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwace mkazi wace;

26. cimodzimodzi waciwiri, ndi wacitatu, kufikira wacisanu ndi ciwiri.

27. Ndipo pomarizira anamwaliranso mkaziyo.

28. Cifukwa cace m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? pakuti onse anakhala naye.

29. Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa a osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.

30. Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.

31. Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi comwe cinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,

32. Ine ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.

33. Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi ciphunzitso cace.

34. Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.

35. Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,

36. Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?

37. Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

Mateyu 22