43. Cifukwa cace ndinena kwa inu, 2 Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zace.
44. Ndipo 3 iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.
45. Ndipo ansembe akuru ndi Afarisi, pakumva mafanizo ace, anazindikira kuti alikunena za iwo.
46. Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, 4 cifukwa anamuyesa mneneri.