14. Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womarizira monga kwa iwe.
15. Sikuloleka kwa ine kodi kucita cimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi cifukwa ine ndiri wabwino?
16. Comweco omarizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omarizira.