Mateyu 2:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pa kubadwa kwace kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,

2. nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

3. Ndipo Herode mfumuyo pakumva ici anabvutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.

Mateyu 2