Mateyu 19:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anacokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.

2. Ndipo makamu akuru a anthu anamtsata; ndipo Iye anawaciritsa kumeneko.

3. Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace pa cifukwa ciri conse?

4. Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu paciyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,

5. nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?

6. cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.

7. Iwo ananena kwa Iye, Nanga cifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa cilekaniro, ndi kumcotsa?

8. Iye ananena kwa iwo, Cifukwa ca kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kucotsa akazi anu; koma paciyambi sikunakhala comweco.

9. Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akacotsa mkazi wace, kosakhala cifukwa ca cigololo, nadzakwatira wina, acita cigololo: ndipo iye amene akwatira wocotsedwayo, acita cigololo.

10. Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wace uti wotere, sikuli kwabwino kukwatira.

Mateyu 19