Mateyu 18:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?

2. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,

3. nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

4. Cifukwa cace yense amene adzicepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

5. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka cifukwa ca dzina langa, alandira Ine;

6. koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikuru ikolowekedwe m'khosi mwace, namizidwe poya pa nyanja.

7. Tsoka liri hdi dziko lapansi cifukwa ca zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene cokhumudwitsaco cidza ndi iye.

Mateyu 18