4. Pakuti Mulungu anati,Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo,Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.
5. Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu;
6. iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.
7. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti,
8. Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.
9. Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
10. Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;
11. si cimene cilowa m'kamwa mwace ciipitsa munthu; koma cimene cituruka m'kamwa mwace, ndico ciipitsa munthu.
12. Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva conenaco?
13. Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzala, udzazulidwa.
14. Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.
15. Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli.
16. Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala cipulukirire?
17. Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo?