3. Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu?
4. Pakuti Mulungu anati,Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo,Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.
5. Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu;
6. iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.
7. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti,
8. Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.
9. Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
10. Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;
11. si cimene cilowa m'kamwa mwace ciipitsa munthu; koma cimene cituruka m'kamwa mwace, ndico ciipitsa munthu.
12. Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva conenaco?