Mateyu 14:33-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.

34. Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete.

35. Ndipo m'meneamuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse ku dziko lonse lozungulira, nadzanao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda;

36. ndipo anampempha Iye, kuti akhudze yokha mphonje ya cobvala cace; ndipo onse amene anamkhudza anaciritsidwa.

Mateyu 14