9. ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;
10. ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;
11. ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.
12. Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele;
13. ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
14. ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;