Mateyu 1:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. ndi Solomo anabala Rehabiamu; ndi Rehabiamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;

8. ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;

9. ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;

10. ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;

11. ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.

12. Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele;

13. ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;

14. ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;

15. ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;

16. ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa iye.

17. Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi ndi inai.

18. Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

Mateyu 1