22. Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
23. Onani namwali adzaima,Nadzabala mwana wamwamuna,Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli;ndilo losandulika, Mulungu nafe.
24. Ndipo Yosefe anauka tulo tace, nacita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wace;
25. ndipo sanamdziwa iye kufikira atabala rriwana wace; namucha dzina lace Yesu.