Mateyu 1:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

2. Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ace;

3. ndi Yuda anabala Farese ndi Zara mwa Tamare; ndi Farese anabala Ezronu; ndi Ezronu anabala Aramu;

4. ndi Aramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni;

5. ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese;

6. ndi Jese anabala Davide mfumuyo.Ndipo Davide anabala Solomo mwa mkazi wa Uriya;

7. ndi Solomo anabala Rehabiamu; ndi Rehabiamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;

8. ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;

9. ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;

10. ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;

11. ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.

12. Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele;

13. ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;

14. ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;

15. ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;

Mateyu 1