1. Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
2. Yehova ndiye wamkuru m'Ziyoni;Ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3. Alemekeze dzina lanu lalikuru ndi loopsa;Ili ndilo loyera.
4. Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda ciweruzo;Inu mukhazikitsa zolunjika,Mucita ciweruzo ndi cilungamo m'Yakobo.