Masalmo 90:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mamawa uphuka bwino;Madzulo ausenga, nuuma.

7. Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu;Ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa.

8. Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,Ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.

9. Pakuti masiku athu onse apitirira m'ukali wanu;Titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.

10. Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri,Kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu;Koma teronso kukula kwao kumati cibvuto ndi copanda pace;Pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.

11. Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,Ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

12. Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,Kuti tikhale nao mtima wanzeru.

Masalmo 90