6. Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse;Ndipo midziyo mwaipasula,Cikumbukilo cao pamodzi catha.
7. Koma Yehova akhala cikhalire:Anakonzeratu mpando wacifumu wace kuti aweruze.
8. Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'cilungamo,Nadzaweruza anthu molunjika.
9. Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi.Msanje m'nyengo za nsautso;
10. Ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu;Pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.
11. Yimbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni;Lalikirani mwa anthu nchito zace.
12. Pakuti Iye wofuna camwazi awakumbukila;Saiwala kulira kwa ozunzika.
13. Ndicitireni cifundo, Yehova;Penyani kuzunzika kwanga kumene andicitira ondidawo,Inu wondinyamula kundicotsa ku zipata za imfa;
14. Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;Pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,Ndidzakondwera naco cipulumutso canu.
15. Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba:Lakodwa phazi lao muukonde anaucha.
16. Anadziwika Yehova, anacita kuweruza:Woipayo anakodwa ndi nchito ya manja ace.
17. Oipawo adzabwerera kumanda,Inde amitundu onse akuiwala Mulungu.