Masalmo 89:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Munalenga kumpoto ndi kumwela;Tabora ndi Hermoni apfuula mokondwera m'dzina lanu.

13. Muli nao mkono wanu wolimba;M'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.

14. Cilungamo ndi ciweruzo ndiwo maziko a mpando wacifumu wanu;Cifundo ndi coonadi zitsogolera pankhope panu.

15. Odala anthu odziwa liu la lipenga;Ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Masalmo 89