Masalmo 83:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Monga moto upsereza nkhalango,Ndi monga lawi liyatsa mapiri;

15. Momwemo muwatsate ndi namondwe,Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.

16. Acititseni manyazi pankhope pao;Kuti afune dzina lanu, Yehova.

17. Acite manyazi, naopsedwe kosatha;Ndipo asokonezeke, naonongeke:

18. Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,Ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Masalmo 83