5. Anaciika cikhale mboni kwa Yosefe,Pakuturuka iye ku dziko la Aigupto:Komwe ndinamva cinenedwe cosadziwa ine.
6. Ndinamcotsera katundu paphewa pace:Manja ace anamasuka kucotengera.
7. Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;Ndinakubvomereza mobisalika m'bingu;Ndinakuyesa ku madzi a Meriba.
8. Tamvani, anthu anga, ndidzakucitirani mboni;Israyeli, ukadzandimvera!
9. Kwanu kusakhale mulungu wafuma kwina;Nusagwadire mulungu wacilendo.