Masalmo 81:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yimbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu;Pfuulirani kwa Mulungu wa Yakobo.

2. Utsani Salimo, bwera nakoni kalingaka,Zeze wokondwetsa pamodzi ndi cisakasa.

3. Ombani lipenga, pokhala mwezi,Utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.

4. Pakuti ici ndi colemba ca kwa Israyeli,Ciweruzo ca Mulungu wa Yakobo.

Masalmo 81