Masalmo 80:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaokaeNdi mphanda munadzilimbikitsira.

16. Unapserera ndi moto, unadulidwa;Aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

17. Dzanja lanu likhale pa munthu wa pa dzanja lamanja lanu;Pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

18. Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani;Titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.

19. Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

Masalmo 80