Masalmo 8:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti munamcepsa pang'ono ndi Mulungu,Munambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

6. Munamcititsa ufumu pa nchito za manja anu;Mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace;

7. Nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo,Ndi nyama za kuthengo zomwe;

8. Mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja.Zopita m'njira za m'nyanja.

9. Yehova, Ambuye wathu,Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!

Masalmo 8