Masalmo 78:58-61 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

58. Ndipo anautsa mtima wace ndi malo amsanje ao,Namcititsa nsanje ndi mafano osema.

59. Pakumva ici Mulungu, anakwiya, Nanyozatu Israyeli;

60. Ndipo anacokera cokhalamo ca ku Silo,Cihemaco adacimanga mwa anthu;

61. Napereka mphamvu yace m'ukapolo,Ndi ulemerero wace m'dzanja la msautsi.

Masalmo 78