49. Anawatumizira mkwiyo wace wotentha,Kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso,Ndizo gulu la amithenga ocita zoipa.
50. Analambulira mkwiyo wace njira;Sanalekerera moyo wao usafe,Koma anapereka moyo wao kumliri;
51. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Aigupto,Ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu:
52. Koma anaturutsa anthu ace ngati nkhosa,Nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'cipululu.
53. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika,Kotero kuti sanaopa;Koma nyanja inamiza adani ao.
54. Ndipo anawafikitsa ku malire a malo ace oyera,Ku phiri ili, dzanja lamanja lace lidaligula.
55. Ndipo anapitikitsa amitundu pamaso pao,Nawagawira colowa cao, ndi muyeso,Nakhalitsa mafuko a Israyeli m'mahema mwao.
56. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba,Osasunga mboni zace;