36. Koma anamsyasyalika pakamwa pao,Namnamiza ndi lilime lao.
37. Popeza mtima wao sunakonzekera Iye,Ndipo sanakhazikika m'cipangano cace.
38. Koma Iye pokhala ngwa cifundo,Anakhululukira coipa, osawaononga;Nabweza mkwiyo wace kawiri kawiri,Sanautsa ukali wace wonse.
39. Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu;Mphepo yopita yosabweranso.
40. Kawiri kawiri nanga anapikisana ndi Iye kucigwako,Nammvetsa cisoni m'cipululu.