17. Koma anaonjeza kuincimwira Iye,Kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'cipululu.
18. Ndipo anayesa Mulungu mumtimamwaoNdi kupempha cakudya monga mwa kulakalaka kwao.
19. Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;Anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'cipululu?
20. Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendakoNdi mitsinje inasefuka;Kodi adzakhozanso kupatsa mkate?Kodi adzafunira anthu ace nyama?
21. Cifukwa cace Yehova anamva, nakwiya;Ndipo anayatsa moto pa Yakobo,Ndiponso mkwiyo unakwera pa Israyeli;
22. Popeza sanakhulupirira Mulungu,Osatama cipulumutso cace.
23. Koma analamulira mitambo iri m'mwamba,Natsegula m'makomo a kumwamba.