1. Tamverani, anthu anga, cilamulo canga;Cherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.
2. Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira;Ndidzachula zinsinsi zoyambira kale;
3. Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa,Ndipo makolo athu anatifotokozera.
4. Sitidzazibisira ana ao,Koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova,Ndi mphamvu yace, ndi zodabwiza zace zimene anazicita.