Masalmo 77:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Madziwo anakuonani Mulungu;Anakuonani madziwo; anacita mantha:Zozama zomwe zinanjenjemera,

17. Makongwa anatsanula madzi;Thambo lidamvetsa liu lace;Mibvi yanu yomwe inaturukira.

18. Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;Mphezi zinaunikira ponse pali anthu;Dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

19. Njira yanu inali m'nyanja,Koyenda Inu nku madzi akulu,Ndipo mapazi anu sanadziwika.

20. Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa,Ndi dzanja la Mose ndi Aroni,

Masalmo 77