Masalmo 76:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuuka Mulungu kuti aweruze,Kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.

10. Indedi, kuzaza kwace kwa munthu kudzakulemekezani;Cotsalira ca kuzazaku mudzaciletsa.

11. Windani ndipo citirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;Onse akumzinga abwere naco copereka ca kwa Iye amene ayenera kumuopa.

12. Iye adzadula mzimu wa akulu;Akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.

Masalmo 76