Masalmo 73:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Sabvutika monga anthu ena;Sasautsika monga anthu ena.

6. Cifukwa cace kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;Acibvala ciwawa ngati malaya.

7. Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao:Malingaliro a mitima yao asefukira.

8. Acita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa:Alankhula modzitama.

9. Pakamwa pao anena zam'mwamba,Ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.

Masalmo 73