Masalmo 71:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;Mwalamulira kundipulumutsa;Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

4. Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,M'dzanja la munthu wosalungama ndi waciwawa.

5. Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova;Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

6. Inu munandigwirizizakuyambira ndisanabadwe:Kuyambira pa thupi la mai wanga wondicitira zokoma ndinu;Ndidzakulemekezani kosalekeza.

7. Ndikhala codabwiza kwa ambiri;Koma Inu ndinu pothawira panga polimba.

8. M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,Ndi ulemu wanu tsiku lonse.

Masalmo 71