Masalmo 69:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,

8. Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9. Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.

11. Ndipo cobvala canga ndinayesa ciguduli,Koma amandiphera mwambi.

12. Okhala pacipata akamba za ine; Ndipo oledzera andiyimba.

Masalmo 69