Masalmo 68:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Inu, Mulungu, munabvumbitsa cimvula,Munatsitsimutsa colowa canu pamene cidathodwa.

10. Gulu lanu linakhala m'dziko muja:Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.

11. Ambuye anapatsa mau:Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikuru.

12. Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa:Ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

13. Pogona inu m'makola a zoweta,Mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva,Ndi nthenga zace zokulira ndi golidi woyenga wonyezimira.

14. Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo,Munayera ngati matalala m'Salimoni.

15. Phiri la Basana ndilo phiri la Mulungu;Phiri la Basana ndilo phiri la mitu mitu.

16. Mucitiranji nsanje mapiri inu a mitu mitu,Ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

17. Magareta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikiza-wirikiza:Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika,

18. Munakwera kumka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende;Munalandira zaufulu mwa anthu,Ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.

Masalmo 68