Masalmo 68:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Auke Mulungu, abalalike adani ace;Iwonso akumuda athawe pamaso pace.

2. Muwacotse monga utsi ucotseka; Monga phula lisungunuka pamoto,Aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.

3. Koma olungama akondwere; atumphe ndi cimwemwe pamaso pa Mulungu;Ndipo asekere naco cikondwerero.

Masalmo 68