Masalmo 63:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;Ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

5. Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;Ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakupfuula mokondwera;

6. Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

7. Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

8. Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

9. Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.

10. Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.

Masalmo 63