Masalmo 6:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndalema nako kuusa moyo kwanga;Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;Mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

7. Lapuwala diso langa cifukwa ca cisoni;Lakalamba cifukwa ca onse akundisautsa.

8. Cokani kwa ine, nonsenu akucita zopanda pace;Pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanaa,

9. Wamva Yehova kupemba kwanga;Yehova adzalandira pemphero langa.

10. Adzacita manyazi, nadzanthunthumira kwakukuru adani anga onse;Adzabwerera, nadzacita manyazi modzidzimuka,

Masalmo 6