Masalmo 59:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti onani, alalira moyo wanga;Amphamvu andipangira ciwembu:Osacimwa, osalakwa ine, Yehova,

4. Osawapatsa cifukwa ine, athamanga nadzikonza;Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.

5. Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli,Ukani kukazonda amitundu onse:Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.

6. Abwera madzulo, auwa ngati garu,Nazungulira mudzi.

7. Onani abwetuka pakamwa pao;M'milomo mwao muli lupanga,Pakuti amati, Amva ndani?

Masalmo 59