11. Musawapheretu, angaiwale anthu anga:Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,Ambuye, ndinu cikopa cathu.
12. Pakamwa pao acimwa ndi mau onse a pa milomo yao,Potero akodwe m'kudzitamandira kwao,Ndiponso cifukwa ca kutemberera ndi bodza azilankhula.
13. Muwathe mumkwiyo, muwagurule psiti:Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo,Kufikira malekezero a dziko la pansi.
14. Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,Nazungulire mudzi.
15. Ayendeyende ndi kufuna cakudya,Nacezere osakhuta.