Masalmo 51:17-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

18. Citirani Ziyoni cokoma monga mwa kukondwera kwanu;Mumange malinga a miyala a Yerusalemu.

19. Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zacilungamo,Ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu:Pamenepo adzaperekaNg'ombe pa guwa lanu la nsembe.

Masalmo 51