Masalmo 50:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndikamva njala, sindidzakuuza:Pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwace komwe.

13. Kodi ndidzadya nyama ya ng'ombe,Kapena kumwa mwazi wa mbuzi?

14. Pereka kwa Mulungu nsembe yaciyamiko;Numcitire Wam'mwambamwamba cowinda cako:

15. Ndipo undiitane tsiku la cisautso:Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

16. Koma kwa woipa Mulungu anena,Uli nao ciani malemba anga kulalikira,Ndi kuchula pangano langa pakamwa pako?

17. Popeza udana naco cilangizo,Nufulatira mau anga.

Masalmo 50