Masalmo 49:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndidzachera khutu kufanizo:Ndidzafotokozera cophiphiritsa canga poyimbira.

5. Ndidzaoperanji masiku oipa,Pondizinga amphulupulu onditsata kucidendene?

6. Iwo akutama kulemera kwao;Nadzitamandira pa kucuruka kwa cuma cao;

7. Kuombola mbale sangadzamuombole,Kapena kumperekera dipo kwa Mulungu:

8. (Popeza ciombolo ca moyo wao nca mtengo wace wapatali,Ndipo cilekeke nthawi zonse)

Masalmo 49