1. Pakupfuula ine mundiyankhe, Mulungu wa cilungamo canga;Pondicepera mwandikulitsira malo:Ndicitireni cifundo, imvani pemphero langa.
2. Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?Mudzakonda zacabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
3. Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayoAdzamva Yehova m'mene ndimpfuulira Iye,