6. Munthu uyu wozunzika anapfuula, ndipo Yehova anamumva,Nampulumutsa m'masautso ace onse.
7. Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye,Nawalanditsa iwo.
8. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.
9. Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.
10. Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.
11. Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.
12. Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?
13. Uletse lilime lako lisachule zoipa,Ndipo milomo yako isalankhule cinyengo.