19. Masautso a wolungama mtima acuruka:Koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.
20. Iye asunga mafupa ace onse:Silinatyoka limodzi lonse.
21. Mphulupulu idzamupha woipa:Ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.
22. Yehova aombola moyo wa anyamata ace,Ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.