Masalmo 34:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtimawosweka,Apulumutsa iwo a mzimu wolapadi,

19. Masautso a wolungama mtima acuruka:Koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

20. Iye asunga mafupa ace onse:Silinatyoka limodzi lonse.

21. Mphulupulu idzamupha woipa:Ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

22. Yehova aombola moyo wa anyamata ace,Ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.

Masalmo 34