Masalmo 33:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;Analamulira, ndipo cinakhazikika.

10. Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11. Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

12. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.

Masalmo 33